16 Nchito za wolungama zipatsa moyo;Koma phindu la oipa licimwitsa.
17 Wosunga mwambo ali m'njira ya moyo;Koma wosiya cidzudzulo asocera.
18 Wobisa udani ali ndi milomo yonama;Wonena ugogodi ndiye citsiru.
19 Pocuruka mau zolakwa sizisoweka;Koma wokhala cete acita mwanzeru.
20 Lilime la wolungama likunga siliva wosankhika;Koma mtima wa oipa uli wacabe.
21 Milomo ya wolungama imadyetsa ambiri;Koma zitsiru zimafa posowa nzeru.
22 Madalitso a Yehova alemeretsa,Saonjezerapo cisoni.