1 Wokonda mwambo akonda kudziwa;Koma wakuda cidzudzulo apulukira.
2 Yehova akomera mtima munthu wabwino;Koma munthu wa ziwembu amtsutsa,
3 Munthu sadzakhazikika ndi udio,Muzu wa olungama sudzasunthidwa.
4 Mkazi wodekha ndiye korona wa mwamuna wace;Koma wocititsa manyazi akunga cobvunditsa mafupa a mwamunayo.
5 Maganizo a olungama ndi ciweruzo;Koma uphungu wa oipa unyenga.
6 Mau a oipa abisalira mwazi;Koma m'kamwa mwa olungama muwalanditsa.