14 Munthu amakhuta zabwino ndi zipatso za m'kamwa mwace;Zocita za manja ace zidzabwezedwa kwa iye.
15 Njira ya citsiru nlolungama pamaso pace pace;Koma wanzeru amamvera uphungu.
16 Mkwiyo wa citsiru udziwika posacedwa;Koma wanzeru amabisa manyazi.
17 Wolankhula ntheradi aonetsa cilungamo;Koma mboni yonama imanyenga.
18 Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga;Koma lilime la anzeru lilamitsa.
19 Mlomo wa ntheradi ukhazikika nthawi zonse;Koma lilime lonama likhala kamphindi.
20 Cinyengo ciri m'mitima ya oganizira zoipa;Koma aphungu a mtendere amakondwa.