17 Wolankhula ntheradi aonetsa cilungamo;Koma mboni yonama imanyenga.
18 Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga;Koma lilime la anzeru lilamitsa.
19 Mlomo wa ntheradi ukhazikika nthawi zonse;Koma lilime lonama likhala kamphindi.
20 Cinyengo ciri m'mitima ya oganizira zoipa;Koma aphungu a mtendere amakondwa.
21 Palibe bvuto lidzagwera wolungama;Koma amphulupulu adzadzazidwa ndi zoipa,
22 Milomo yonama inyansa Yehova;Koma ocita ntheradi amsekeretsa.
23 Munthu wanzeru abisa zomwe adziwa;Koma mtima wa opusa ulalikira utsiru.