19 Mlomo wa ntheradi ukhazikika nthawi zonse;Koma lilime lonama likhala kamphindi.
20 Cinyengo ciri m'mitima ya oganizira zoipa;Koma aphungu a mtendere amakondwa.
21 Palibe bvuto lidzagwera wolungama;Koma amphulupulu adzadzazidwa ndi zoipa,
22 Milomo yonama inyansa Yehova;Koma ocita ntheradi amsekeretsa.
23 Munthu wanzeru abisa zomwe adziwa;Koma mtima wa opusa ulalikira utsiru.
24 Dzanja la akhama lidzalamulira;Koma wolesi adzakhala ngati kapolo,
25 Nkhawa iweramitsa mtima wa munthu;Koma mau abwino aukondweretsa.