22 Milomo yonama inyansa Yehova;Koma ocita ntheradi amsekeretsa.
23 Munthu wanzeru abisa zomwe adziwa;Koma mtima wa opusa ulalikira utsiru.
24 Dzanja la akhama lidzalamulira;Koma wolesi adzakhala ngati kapolo,
25 Nkhawa iweramitsa mtima wa munthu;Koma mau abwino aukondweretsa.
26 Wolungama atsogolera mnzace;Koma njira ya oipa iwasokeretsa.
27 Wolesi samaocha nyama yace anaigwira;Koma wolungama amalandira cuma copambana ca anthu.
28 M'khwalala la cilungamo muli moyo;M'njira ya mayendedwe ace mulibe imfa.