1 Malongosoledwe a mtima nga munthu;Koma mayankhidwe a lilime acokera kwa Yehova.
2 Njira zonse za munthu ziyera pamaso pace;Koma Yehova ayesa mizimu.
3 Pereka zocita zako kwa Yehova,Ndipo zolingalira zako zidzakhazikika.
4 Zonse Yehova anazipangaziri ndi zifukwa zao;Ngakhale amphulupulu kuti aone tsiku loipa,
5 Yense wonyada mtima anyansa Yehova;Zoonadi sadzapulumuka cilango.
6 Mphulupulu iomboledwa ndi cifundo ndi ntheradi;Apatuka pa zoipa poopa Yehova.