11 Mwini muyeso ndi mulingo wolungama ndiye Yehova;Ndiyenso anapanga miyala yonse yoyesera ya m'thumba.
12 Kucita mphulupulu kunyansa mafumu;Pakuti mpando wao wakhazikika ndi cilungamo.
13 Milomo yolungama ikondweretsa mafumu;Wonena zoongoka amkonda.
14 Mkwiyo wa mfumu ndi mithenga ya imfa;Wanzeru adzaukhulula.
15 M'kuunika kwa nkhope ya mfumu muli moyo;Kukoma mtima kwace kunga mtambo wa mvula ya masika.
16 Kodi kulandira nzeru sikupambana ndi golidi,Kulandira luntha ndi kusankhika koposa siliva?
17 Khwalala la oongoka mtima ndilo lakuti asiye zoipa;Wosunga njira yace acinjiriza moyo wace.