12 Kucita mphulupulu kunyansa mafumu;Pakuti mpando wao wakhazikika ndi cilungamo.
13 Milomo yolungama ikondweretsa mafumu;Wonena zoongoka amkonda.
14 Mkwiyo wa mfumu ndi mithenga ya imfa;Wanzeru adzaukhulula.
15 M'kuunika kwa nkhope ya mfumu muli moyo;Kukoma mtima kwace kunga mtambo wa mvula ya masika.
16 Kodi kulandira nzeru sikupambana ndi golidi,Kulandira luntha ndi kusankhika koposa siliva?
17 Khwalala la oongoka mtima ndilo lakuti asiye zoipa;Wosunga njira yace acinjiriza moyo wace.
18 Kunyada kutsogolera kuonongekaMtinia wodzikuza ndi kutsogolera kupunthwa.