16 Kodi kulandira nzeru sikupambana ndi golidi,Kulandira luntha ndi kusankhika koposa siliva?
17 Khwalala la oongoka mtima ndilo lakuti asiye zoipa;Wosunga njira yace acinjiriza moyo wace.
18 Kunyada kutsogolera kuonongekaMtinia wodzikuza ndi kutsogolera kupunthwa.
19 Kufatsa mtima ndi osaukaKuposa kugawana zofunkha ndi onyada.
20 Wolabadira mau adzapeza bwino;Ndipo wokhulupirira Yehova adala.
21 Wanzeru mtima adzachedwa wocenjera;Ndipo kukoma kwa milomo kuyenjezera kuphunzira.
22 Nzeru ndi kasupe wa moyo kwa mwini wace;Koma mwambo wa zitsiru ndi utsiru.