2 Njira zonse za munthu ziyera pamaso pace;Koma Yehova ayesa mizimu.
3 Pereka zocita zako kwa Yehova,Ndipo zolingalira zako zidzakhazikika.
4 Zonse Yehova anazipangaziri ndi zifukwa zao;Ngakhale amphulupulu kuti aone tsiku loipa,
5 Yense wonyada mtima anyansa Yehova;Zoonadi sadzapulumuka cilango.
6 Mphulupulu iomboledwa ndi cifundo ndi ntheradi;Apatuka pa zoipa poopa Yehova.
7 Njira za munthu zikakonda Yehova,Ayanjanitsana naye ngakhale adani ace.
8 Zapang'ono, pokhala cilungamo,Ziposa phindu lalikuru lopanda ciweruzo.