22 Nzeru ndi kasupe wa moyo kwa mwini wace;Koma mwambo wa zitsiru ndi utsiru.
23 Mtima wa wanzeru ucenjeza m'kamwa mwace,Nuphunzitsanso milomo yace.
24 Mau okoma ndiwo cisa ca uci,Otsekemera m'moyo ndi olamitsa mafupa.
25 Iripo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka,Koma matsiriziro ace ndi njira za imfa.
26 Wanchito adzigwirira yekha nchito;Pakuti m'kamwa mwace mumfulumiza.
27 Munthu wopanda pace akonzeratu zoipa;Ndipo m'milomo mwace muli moto wopsereza.
28 Munthu wokhota amautsa makani;Kazitape afetsa ubwenzi.