28 Munthu wokhota amautsa makani;Kazitape afetsa ubwenzi.
29 Munthu waciwawa akopa mnzace,Namuyendetsa m'njira yosakhala bwino.
30 Wotsinzina ndiye aganizira zakhota;Wosunama afikitsa zoipa.
31 Imvi ndiyo korona wa ulemu,Idzapezedwa m'njira ya cilungamo.
32 Wosakwiya msanga aposa wamphamvu;Wolamulira mtima wace naposa wolanda mudzi.
33 Maere aponyedwa pamfunga;Koma ndiye Yehova alongosola zonse.