4 Zonse Yehova anazipangaziri ndi zifukwa zao;Ngakhale amphulupulu kuti aone tsiku loipa,
5 Yense wonyada mtima anyansa Yehova;Zoonadi sadzapulumuka cilango.
6 Mphulupulu iomboledwa ndi cifundo ndi ntheradi;Apatuka pa zoipa poopa Yehova.
7 Njira za munthu zikakonda Yehova,Ayanjanitsana naye ngakhale adani ace.
8 Zapang'ono, pokhala cilungamo,Ziposa phindu lalikuru lopanda ciweruzo.
9 Mtima wa munthu ulingalira njira yace;Koma Yehova ayendetsa mapazi ace.
10 Mau a mlauli ali m'milomo ya mfumu;M'kamwa mwace simudzacita cetera poweruza.