1 Nyenyeswa youma, pokhala mtendere,Iposa nyumba yodzala nyama yansembe, pali makangano.
2 Kapolo wocitamwanzeruAdzalamulira mwana wocititsa manyazi,Nadzagawana nao abale colowa.
3 Siliva ali ndi mbiya yosungunulira, golidi ali ndi ng'anjo;Koma Yehova ayesa mitima.
4 Wocimwa amasamalira milomo yolakwa;Wonama amvera lilime losakaza.