1 Nyenyeswa youma, pokhala mtendere,Iposa nyumba yodzala nyama yansembe, pali makangano.
2 Kapolo wocitamwanzeruAdzalamulira mwana wocititsa manyazi,Nadzagawana nao abale colowa.
3 Siliva ali ndi mbiya yosungunulira, golidi ali ndi ng'anjo;Koma Yehova ayesa mitima.
4 Wocimwa amasamalira milomo yolakwa;Wonama amvera lilime losakaza.
5 Wocitira ciphwete aumphawi atonza Mlengi;Wokondwera ndi tsoka sadzapulumuka cilango.
6 Zidzukulu ndizo korona wa okalamba;Ndipo ulemerero wa ana ndiwo atate ao.
7 Mlomo wangwiro suyenera citsiru;Ngakhale mlomo wonama suyenera kalonga ndi pang'ono ponse.