10 Cidzudzulo cilowa m'kati mwa wozindikira,Kopambana ndi kukwapula wopusa kwambiri.
11 Woipa amafuna kupanduka kokha;Koma adzamtumizira mthenga wankhanza.
12 Kukomana ndi citsiru m'kupusa kwaceKuopsya koposa cirombo cocicotsera anace.
13 Wobwezera zabwino zoipa,Zoipa sizidzamcokera kwao.
14 Ciyambi ca ndeu cifanana ndi kutsegulira madzi;Tsono kupikisana kusanayambe tasiya makani.
15 Wokometsa mlandu wa wamphulupulu, ndi wotsutsa wolungama,Onse awiriwa amnyansa Yehova.
16 Kodi bwanji mtengo wogulira nzeru uli m'dzanja la citsiru,Popeza wopusa alibe mtima?