16 Kodi bwanji mtengo wogulira nzeru uli m'dzanja la citsiru,Popeza wopusa alibe mtima?
17 Bwenzi limakonda nthawi zonse;Ndipo mbale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.
18 Munthu wosowa nzeru apangana kulipirira wina,Napereka cikole pamaso pa mnzace.
19 Wokonda ndeu akonda kulakwa;Ndipo wotarikitsa khomo lace afunafuna kuonongeka.
20 Wokhota mtima sadzapeza bwinoNdipo mwini lilime lokhota adzagwa m'zoipa.
21 Wobala citsiru adzicititsa cisoni;Ndipo atate wa wopusa sakondwa.
22 Mtima wosekerera uciritsa bwinoKoma mzimu wosweka uphwetsa mafupa,