20 Wokhota mtima sadzapeza bwinoNdipo mwini lilime lokhota adzagwa m'zoipa.
21 Wobala citsiru adzicititsa cisoni;Ndipo atate wa wopusa sakondwa.
22 Mtima wosekerera uciritsa bwinoKoma mzimu wosweka uphwetsa mafupa,
23 Munthu woipa alandira cokometsera mlandu coturutsa m'mfunga,Kuti apambukitse mayendedwe a ciweruzo.
24 Nzeru iri pamaso pa wozindikira;Koma maso a wopusa ali m'malekezero a dziko.
25 Mwana wopusa acititsa atate wace cisoni,Namvetsa zowawa amace wombala.
26 Kulipiritsa wolungama sikuli kwabwino,Ngakhale kukwapula akuru cifukwa aongoka mtima.