6 Zidzukulu ndizo korona wa okalamba;Ndipo ulemerero wa ana ndiwo atate ao.
7 Mlomo wangwiro suyenera citsiru;Ngakhale mlomo wonama suyenera kalonga ndi pang'ono ponse.
8 Wolandira cokometsera mlandu aciyesa ngale;Pali ponse popita iye acenjera.
9 Wobisa colakwa afunitsa cikondano;Koma wobwereza-bwereza mau afetsa ubwenzi.
10 Cidzudzulo cilowa m'kati mwa wozindikira,Kopambana ndi kukwapula wopusa kwambiri.
11 Woipa amafuna kupanduka kokha;Koma adzamtumizira mthenga wankhanza.
12 Kukomana ndi citsiru m'kupusa kwaceKuopsya koposa cirombo cocicotsera anace.