1 Wopanduka afunafuna niro cace,Nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.
2 Wopusa sakondwera ndi kuzindikira;Koma kungobvumbulutsa za m'mtima mwace.
3 Pakudza wamphulupulu padzanso kunyoza;Manyazi natsagana ndi citonzo.
4 Mau a m'kamwa mwa munthu ndiwo madzi akuya;Kasupe wa nzeru ndiye mtsinje wodzala.
5 Kukometsa mlandu wa wamphulupulu mwatsankhu sikuli kwabwino,Ngakhale kucitira cetera wolungama.
6 Milomo ya wopusa ifikitsa makangano;Ndipo m'kamwa mwace muputa kukwapulidwa.
7 M'kamwa mwa wopusa mumuononga,Milomo yace ikhala msampha wa moyo wace.