11 Cuma ca wolemera ndico mudzi wace wolimba;Alingalira kuti ndico khoma lalitari.
12 Mtima wa munthu unyada asanaonongeke;Koma cifatso citsogolera ulemu.
13 Wobwezera mau asanamvetse apusa,Nadzicititsa manyazi.
14 Mtima wa munthu umlimbitsa alikudwala;Koma ndani angatukule mtima wosweka?
15 Mtima wa wozindikira umaphunzira;Khutu la anzeru lifunitsa kudziwa.
16 Mtulo wa munthu umtsegulira njira,Numfikitsa pamaso pa akuru.
17 Woyamba kudzinenera ayang'anika wolungama;Koma mnzace afika namuululitsa zace zonse.