18 Ula uletsa makangano,Nulekanitsa amphamvu.
19 Kupembedza mbale utamcimwira nkobvuta,Kulanda mudzi wolimba nkosabvuta;Makangano akunga mipiringidzo ya linga.
20 Mimba ya munthu idzakhuta zipatso za m'kamwa mwace;Iye nadzakhuta phindu la milomo yace.
21 Lilime liri ndi mphamvu pa imfa ndi moyo;Wolikonda adzadya zipatso zace.
22 Wopeza mkazi apeza cinthu cabwino;Yehova amkomera mtima.
23 Wosauka amadandaulira;Koma wolemera ayankha mwaukali.
24 Woyanjana ndi ambiri angodziononga;Koma liripo bwenzi lipambana ndi mbale kuumirira.