4 Mau a m'kamwa mwa munthu ndiwo madzi akuya;Kasupe wa nzeru ndiye mtsinje wodzala.
5 Kukometsa mlandu wa wamphulupulu mwatsankhu sikuli kwabwino,Ngakhale kucitira cetera wolungama.
6 Milomo ya wopusa ifikitsa makangano;Ndipo m'kamwa mwace muputa kukwapulidwa.
7 M'kamwa mwa wopusa mumuononga,Milomo yace ikhala msampha wa moyo wace.
8 Mau a kazitape akunga zakudya zolongosoka,Zotsikira m'kati mwa mimba.
9 Wogwira nchito mwaulesiNdiye mbale wace wa wosakaza.
10 Dzina la Yehova ndilo linga lolimba;Wolungama athamangiramo napulumuka.