1 Wosauka woyenda mwangwiroAposa wokhetsa milomo ndi wopusa.
2 Kukhumba kosadziwa sikuli kwabwino;Ndipo wofulumira ndi mapazi ace amacimwa.
3 Utsiru wa munthu ukhotetsa njira yace;Mtima wace udandaula pa Yehova.
4 Cuma cionjezetsa mabwenzi ambiri;Koma mnzace wa waumphawi amleka.
5 Mboni yonama sidzakhala yosalangidwa;Wolankhula mabodza sadzapulumuka.
6 Ambiri adzapembedza waufulu;Ndipo yense ndi bwenzi la munthu wopatsa.
7 Abale onse a wosauka amuda;Nanga mabwenzi ace kodi satanimphirana naye?Awatsata ndi mau, koma kuli zi.