14 Nyumba ndi cuma ndizo colowa ca atate;Koma mkazi wanzeru acokera kwa Yehova.
15 Ulesi ugonetsa tulo tofa nato;Ndipo moyo wamkhongono udzamva njala.
16 Wosunga lamulo asunga moyo wace;Wonyalanyaza mayendedwe ace adzafa.
17 Wocitira waumphawi cifundo abwereka Yehova;Adzambwezera cokoma caceco.
18 Menya mwanako, ciyembekezero ciripo,Osafunitsa kumuononga.
19 Munthu waukali alipire mwini;Pakuti ukampulumutsa udzateronso.
20 Tamvera uphungu, nulandire mwambo,Kuti ukhale wanzeru pa cimariziro cako,