4 Cuma cionjezetsa mabwenzi ambiri;Koma mnzace wa waumphawi amleka.
5 Mboni yonama sidzakhala yosalangidwa;Wolankhula mabodza sadzapulumuka.
6 Ambiri adzapembedza waufulu;Ndipo yense ndi bwenzi la munthu wopatsa.
7 Abale onse a wosauka amuda;Nanga mabwenzi ace kodi satanimphirana naye?Awatsata ndi mau, koma kuli zi.
8 Wolandira nzeru akonda moyo wace;Wosunga luntha adzapeza zabwino.
9 Mboni yonama sidzapulumuka cilango;Wolankhula mabodza adzaonongeka.
10 Wopusa sayenera kukhala ndi zinthu zolongosoka;Nanga kapolo ayenera kulamulira akalonga kodi?