9 Mboni yonama sidzapulumuka cilango;Wolankhula mabodza adzaonongeka.
10 Wopusa sayenera kukhala ndi zinthu zolongosoka;Nanga kapolo ayenera kulamulira akalonga kodi?
11 Kulingalira kwa munthu kucedwetsa mkwiyo;Ulemerero wace uli wakuti akhululukire colakwa.
12 Mkwiyo wa mfumu ukunga kubangula kwa mkango;Koma kukoma mtima kwace kunga mame pamsipu.
13 Mwana wopusa ndiye tsoka la atate wace;Ndipo makangano a mkazi ndiwo kudontha-donthabe.
14 Nyumba ndi cuma ndizo colowa ca atate;Koma mkazi wanzeru acokera kwa Yehova.
15 Ulesi ugonetsa tulo tofa nato;Ndipo moyo wamkhongono udzamva njala.