1 Mwananga, ukalandira mau anga,Ndi kusunga malamulo anga;
2 Kucherera makutu ako kunzeru,Kulozetsa mtima wako kukuzindikira;
3 Ukaitananso luntha,Ndi kupfuulira kuti ukazindikire;
4 Ukaifunafuna ngati siliva,Ndi kuipwaira ngati cuma cobisika;
5 Pompo udzazindikira kuopa YehovaNdi kumdziwadi Mulungu.
6 Pakuti Yehova apatsa nzeru;Kudziwa ndi kuzindikira kuturuka m'kamwa mwace;