10 Pakuti nzeru idzalowa m'mtima mwako,Moyo wako udzakondwera ndi kudziwa,
11 Kulingalira kudzakudikira,Kuzindikira kudzakucinjiriza;
12 Kukupulumutsa ku njira yoipa,Kwa anthu onena zokhota;
13 Akusiya mayendedwe olungama,Akayende m'njira za mdima;
14 Omwe asangalala pocita zoipa,Nakondwera ndi zokhota zoipa;
15 Amene apotoza njira zao,Nakhotetsa mayendedwe ao;
16 Nzeru idzakupulumutsa kwa mkazi waciwerewere,Kwa mkazi wacilendo wosyasyalika ndi mau ace;