13 Akusiya mayendedwe olungama,Akayende m'njira za mdima;
14 Omwe asangalala pocita zoipa,Nakondwera ndi zokhota zoipa;
15 Amene apotoza njira zao,Nakhotetsa mayendedwe ao;
16 Nzeru idzakupulumutsa kwa mkazi waciwerewere,Kwa mkazi wacilendo wosyasyalika ndi mau ace;
17 Wosiya bwenzi la ubwana wace,Naiwala cipangano ca Mulungu wace;
18 Nyumba yace itsikira kuimfa,Ndi mayendedwe ace kwa akufa;
19 Onse akunka kwa iye sabweranso,Safika ku njira za moyo;