2 Kucherera makutu ako kunzeru,Kulozetsa mtima wako kukuzindikira;
3 Ukaitananso luntha,Ndi kupfuulira kuti ukazindikire;
4 Ukaifunafuna ngati siliva,Ndi kuipwaira ngati cuma cobisika;
5 Pompo udzazindikira kuopa YehovaNdi kumdziwadi Mulungu.
6 Pakuti Yehova apatsa nzeru;Kudziwa ndi kuzindikira kuturuka m'kamwa mwace;
7 Iye asungira oongoka mtima nzeru yeniyeni;Ndiye cikopa ca oyenda molunjika;
8 Kuti acinjirize njira za ciweruzo,Nadikire khwalala la opatulidwa ace.