5 Pompo udzazindikira kuopa YehovaNdi kumdziwadi Mulungu.
6 Pakuti Yehova apatsa nzeru;Kudziwa ndi kuzindikira kuturuka m'kamwa mwace;
7 Iye asungira oongoka mtima nzeru yeniyeni;Ndiye cikopa ca oyenda molunjika;
8 Kuti acinjirize njira za ciweruzo,Nadikire khwalala la opatulidwa ace.
9 Pamenepo udzazindikira cilungamo ndi ciweruzo,Zolunjika ndi mayendedwe onse abwino.
10 Pakuti nzeru idzalowa m'mtima mwako,Moyo wako udzakondwera ndi kudziwa,
11 Kulingalira kudzakudikira,Kuzindikira kudzakucinjiriza;