1 Vinyo acita ciphwete, cakumwa caukali cisokosa;Wosocera nazo alibe nzeru.
2 Kuopsya kwa mfumu ndiko kubangula kwa mkango;Womputa acimwira moyo wace wace.
3 Kuli ulemu kwa mwamuna kupewa ndeu;Koma zitsiru zonse zimangokangana,
4 Wolesi salima cifukwa ca cisanu;Adzapemphapempha m'masika osalandira kanthu.
5 Uphungu wa m'mtima mwa munthu ndiwo madzi akuya;Koma munthu wozindikira adzatungapo,