17 Zakudya za cinyengo zikondweretsa munthu;Koma pambuyo pace m'kamwa mwace mudzadzala tinsangalabwi.
18 Uphungu utsimikiza zolingalira,Ponya nkhondo utapanga upo.
19 Kazitape woyendayenda awanditsa zinsinsi;Usadudukire woyasama milomo yace.
20 Wotemberera atate wace ndi, amace,Nyali yace idzazima mu mdima woti bi.
21 Colowa cingalandiridwe msanga msanga poyamba pace;Koma citsiriziro cace sicidzadala.
22 Usanene, Ndidzabwezera zoipa;Yembekeza Yehova, adzakupulumutsa.
23 Miyeso yosiyana inyansa Yehova,Ndi mulingo wonyenga suli wabwino.