20 Wotemberera atate wace ndi, amace,Nyali yace idzazima mu mdima woti bi.
21 Colowa cingalandiridwe msanga msanga poyamba pace;Koma citsiriziro cace sicidzadala.
22 Usanene, Ndidzabwezera zoipa;Yembekeza Yehova, adzakupulumutsa.
23 Miyeso yosiyana inyansa Yehova,Ndi mulingo wonyenga suli wabwino.
24 Yehova alongosola mayendedwe a mwamuna;Munthu tsono angazindikire bwanji njira yace?
25 Kunena mwansontho, ici ncopatulika, kuli msampha kwa munthu,Ndi kusinkhasinkha pambuyo pace atawinda.
26 Mfumu yanzeru ipeta amphulupulu,Niyendetsapo njinga ya gareta.