24 Yehova alongosola mayendedwe a mwamuna;Munthu tsono angazindikire bwanji njira yace?
25 Kunena mwansontho, ici ncopatulika, kuli msampha kwa munthu,Ndi kusinkhasinkha pambuyo pace atawinda.
26 Mfumu yanzeru ipeta amphulupulu,Niyendetsapo njinga ya gareta.
27 Mzimu wa munthu ndiwo nyali ya Yehova;Usanthula m'kati monse mwa mimba.
28 Cifundo ndi ntheradi zisunga mfumu;Cifundo cicirikiza mpando wace.
29 Ulemerero wa anyamata ndiwo mphamvu yao;Kukongola kwa nkhalamba ndi
30 Mikwingwirima yopweteka icotsa zoipa;Ndi mikwapulo ilowa m'kati mwa mimba.