5 Uphungu wa m'mtima mwa munthu ndiwo madzi akuya;Koma munthu wozindikira adzatungapo,
6 Anthu ambiri abukitsa yense kukoma mtima kwace;Koma ndani angapeze munthu wokhulupirika?
7 Wolungama woyenda mwangwiro,Anace adala pambuyo pace.
8 Mfumu yokhala pa mpando waweruziraIpitikitsa zoipa zonse ndi maso ace.
9 Ndani anganene, Ndasambitsa mtima wanga,Ndayera opanda cimo?
10 Miyeso yosiyana, ndi malicero osiyana,Zonse ziwirizi zinyansa Yehova.
11 Ngakhale mwana adziwika ndi nchito zace;Ngati nchito yace iri yoyera ngakhale yolungama.