7 Wolungama woyenda mwangwiro,Anace adala pambuyo pace.
8 Mfumu yokhala pa mpando waweruziraIpitikitsa zoipa zonse ndi maso ace.
9 Ndani anganene, Ndasambitsa mtima wanga,Ndayera opanda cimo?
10 Miyeso yosiyana, ndi malicero osiyana,Zonse ziwirizi zinyansa Yehova.
11 Ngakhale mwana adziwika ndi nchito zace;Ngati nchito yace iri yoyera ngakhale yolungama.
12 Khutu lakumva, ndi diso lopenya,Yehova anapanga onse awiriwo.
13 Usakonde tulo ungasauke;Phenyula maso, udzakhuta zakudya.