15 Kucita ciweruzo kukondweretsa wolungama;Koma kuwaononga akucita mphulupulu,
16 Munthu wosocera pa njira ya nzeruAdzakhala m'msonkhano wa akufa.
17 Wokonda zoseketsa adzasauka;Wokonda vinyo ndi mafuta sadzalemera.
18 Wocimwa ndiye ciombolo ca wolungama;Ndipo waciwembu adzalowa m'malo mwa oongoka mtima.
19 Kukhala m'cipululu kufunikaKuposa kukhala ndi mkazi wolongolola ndi wong'ung'udza.
20 Mokhala wanzeru muli katundu wofunika ndi mafuta;Koma wopusa angozimeza.
21 Wolondola cilungamo ndi cifundoApeza moyo, ndi cilungamo, ndi ulemu.