2 Njira zonse za munthu zilungama pamaso pace;Koma Yehova ayesa mitima.
3 Kucita cilungamo ndi ciweruzoKupambana ndi nsembe kumkonda Yehova.
4 Maso akunyada, ndi mtima wodzikuza,Ndi nyali ya oipa, ziri cimo.
5 Zoganizira za wakhama zicurukitsadi katundu;Koma yense wansontho angopeza umphawi.
6 Kupata cuma ndi lilime lonama ndiko nkhungu yoyendayenda, ngakhale misampha ya imfa.
7 Ciwawa ca amphulupulu cidzawakokolola;Cifukwa akana kucita ciweruzo.
8 Wosenza cimo njira yace ikhotakhota;Koma nchito ya woyera mtima ilungama.