25 Cifuniro ca wolesi cimupha;Cifukwa manja ace akana kugwira nchito.
26 Ena asirira modukidwa tsiku lonse;Koma wolungama amapatsa osamana.
27 Nsembe ya oipa inyansa;Makamaka pakudza nayo iwo mwaciwembu.
28 Mboni yonama idzafa;Koma mwamuna wakumvetsa adzanena mosakayika,
29 Munthu woipa aumitsa nkhope yace;Koma woongoka mtima akonza njira zace.
30 Kulibe nzeru ngakhale lunthaNgakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.
31 Kavalo amakonzedweratu cifukwa ca tsiku la nkhondo;Koma wopulumutsa ndiye Yehova.