5 Zoganizira za wakhama zicurukitsadi katundu;Koma yense wansontho angopeza umphawi.
6 Kupata cuma ndi lilime lonama ndiko nkhungu yoyendayenda, ngakhale misampha ya imfa.
7 Ciwawa ca amphulupulu cidzawakokolola;Cifukwa akana kucita ciweruzo.
8 Wosenza cimo njira yace ikhotakhota;Koma nchito ya woyera mtima ilungama.
9 Kukhala pa ngondya ya tsindwi kufunikaKuposa kukhala m'nyumba ndi mkazi wolongolola.
10 Wamphulupulu mtima wace umkhumba zoipa;Sakomera mtima mnzace.
11 Polangidwa wonyoza, wacibwana alandira nzeru,Naphunzira pakuyang'ana pa wanzeru.