14 Monga mitambo ndi mphepo popanda mvula,Momwemo ndiye wodzikweza ndi zipatso zace monyenga.
15 Cipiriro cipembedza mkuru;Lilime lofatsa lityola pfupa,
16 Wapeza uci kodi? Idyapo wokwanira,Kuti ungakukole, nusanze.
17 Phazi lako lilowe m'nyumba ya mnzako kamodzi kamodzi;Kuti angatope nawe ndi kukuda.
18 Wocitira mnzace umboni wonamaNdiye cibonga, ndi lupanga, ndi mubvi wakuthwa.
19 Kukhulupirira munthu wa ciwembu tsiku latsokaKunga dzino lotyoka ndi phazi loguluka.
20 Monga wobvula maraya tsiku lamphepo,Ngakhale kuthira vinyo wosasa m'soda,Momwemo woyimbira nyimbo munthu wacisoni.