1 Monga cipale cofewa m'malimwe, ndi mvula m'masika,Momwemo ulemu suyenera citsiru.
2 Monga mpheta irikuzungulira, ndi namzeze alikuuluka,Momwemo temberero la pacabe silifikira.
3 Cikoti ciyenera kavalo, ndi cam'kamwa ciyenera buru,Ndi ntyole iyenera pamsana pa zitsiru.
4 Usayankhe citsiru monga mwa utsiru wace,Kuti ungafanane naco iwe wekha.