14 Monga citseko cikankhikira pa zitsulo za pamphuthu,Momwemo wolesi agubuduka pakama pace.
15 Wolesi alonga dzanja lace m'mbale;Kumtopetsa kulibweza kukamwa kwace.
16 Wolesi adziyesa wanzeruKoposa anthu asanu ndi awiri akuyankha mozindikira.
17 Wakungopita ndi kubvutika ndi ndeu yosakhala yaceAkunga wogwira makutu a garu.
18 Monga woyaruka woponya nsakali,Mibvi, ndi imfa,
19 Momwemo wonyenga mnzace ndi kuti, Ndi kusewera kumeneku.
20 Posowa nkhuni moto ungozima;Ndi popanda kazitape makangano angoleka.