2 Monga mpheta irikuzungulira, ndi namzeze alikuuluka,Momwemo temberero la pacabe silifikira.
3 Cikoti ciyenera kavalo, ndi cam'kamwa ciyenera buru,Ndi ntyole iyenera pamsana pa zitsiru.
4 Usayankhe citsiru monga mwa utsiru wace,Kuti ungafanane naco iwe wekha.
5 Yankha citsiru monga mwa utsiru wace,Kuti asadziyese wanzeru.
6 Wotumiza mau ndi dzanja la citsiruAdula mapazi ace, namwa zompweteka.
7 Miyendo ya wopunduka iri yolobodoka,Momwemo mwambi m'kamwa mwa zitsiru.
8 Monga thumba la ngale m'mulu wa miyala,Momwemo wocitira citsiru ulemu.