21 Monga makala ozizira pa makala akunyeka, ndi nkhuni pamoto;Momwemo munthu wamakangano autsa ndeu.
22 Mau a kazitape ndi zakudya zolongosokaZitsikira m'kati mwa mimba.
23 Milomo yofunitsitsa ndi mtima woipaIkunga mbale yadothi anaimata ndi mphala yasiliva.
24 Wakuda mnzace amanyenga ndi milomo yace;Koma akundika cinyengo m'kati mwace;
25 Pamene akometsa mau ace usamkhulupirire;Pakuti m'mtima mwace muli zonyansa zisanu ndi ziwiri.
26 Angakhale abisa udani wace pocenjera,Koma udio wace udzabvumbulutsidwa posonkhana anthu.
27 Wokumba dzenje adzagwamo,Wogubuduza mwala, udzabweranso pa iye mwini.