25 Pamene akometsa mau ace usamkhulupirire;Pakuti m'mtima mwace muli zonyansa zisanu ndi ziwiri.
26 Angakhale abisa udani wace pocenjera,Koma udio wace udzabvumbulutsidwa posonkhana anthu.
27 Wokumba dzenje adzagwamo,Wogubuduza mwala, udzabweranso pa iye mwini.
28 Lilime lonama lida omwewo linawasautsa;Ndipo m'kamwa mosyasyalika mungoononga.