7 Miyendo ya wopunduka iri yolobodoka,Momwemo mwambi m'kamwa mwa zitsiru.
8 Monga thumba la ngale m'mulu wa miyala,Momwemo wocitira citsiru ulemu.
9 Monga munga wolasa dzanja la woledzera,Momwemo mwambi m'kamwa mwa zitsiru.
10 Monga woponya mibvi ndi kulasa onse,Momwemo wolembera citsiru, ndi wolembera omwe alikupita panjira.
11 Monga garu abweranso ku masanzi ace,Momwemo citsiru cicitanso zopusa zace.
12 Kodi uona munthu wodziyesa wanzeru?Ngakhale citsiru cidzacenjera koma ameneyo ai.
13 Wolesi ati, Mkango uli panjira,Wobangulawo uli m'makwalala.